KAMBULIRE WATI DEMOCRACY NDILO GWELO LA MAVUTO A ZACHUMA M'DZIKO MUNO*

 


M'busa PPJ Kambulire wa mpingo wa Nsungwi C.C.A.P  omwe uli pansi pa Nkhoma Synod wati, mavuto azachuma omwe dziko lino likudutsamo ndi chifukwa choti a malawi anasankha ulamuliro wa zipani zambiri (Democracy) 


Kambulire wayankhula izi lero pa 19 November 2023 mkati mwa ulaliki wake pa mpingowu. 


Iye anati, pamene dziko lino linali pa ulamuliro wa chipani chimodzi (Dictatorship rule) pansi pa Dr Hastings Kamuzu Banda, ndalama ya dziko lino inali yofanana mphamvu ndi ndalama ya kunja ya dollar ( K1=$1) koma zinthu zinayamba kusintha ndikubwera kwa zipani zambiri pomwe Mtsogoleri aliyese amene wakhala  akusankhidwa ndalama ya kwacha yakhala ikugwa   mphamvu. 


M'busayi watinso kuti ino sinthawi yonena Mtsogoleri wa dziko lino Dr Lazarus Chakwera pa mavuto azachumawa, koma yokangalika kupemphera pakuti tili m'nyengo yomaliza ndipo sanabise kunena kuti olo wina atatenga utsogoleri wa upulezidenti ndalama ya kwacha idzagwabe. 


Kambulire walimbikitsanso a khristu amu Mpingowu kuti  azikhala ndi chikhulipiriro pa Mulungu pa mavuto aliwose amene angakumane nawo , Popereka chitsanzo kuti  ana Israel anali ndi chikhulipiriro kuti awoloka Nyanja atawuzidwa ndi Mulungu kuti adziyenda.


Wolemba: Patrick Chilinda

Edited by: Benjamin GK Nyirenda

Comments

Popular posts from this blog

OUTSTANDING STUDENTS TO BE RECOGNIZED BY PLU

PLU STUDENT UNION ELECTIONS CAMPAIGN DATES CONFIRMED

PLU STUDENT UNION ELECTIONS COMMENCE